BUNGWE LA ATUMIKI ACHIFUNDO LIYAMBA NTCHITO YAKE POFIKIRA A SISTERI A POOR CLARE
- Communications
- Mar 9, 2024
- 1 min read
Updated: Nov 1

Bungwe la Atumiki a Chifundo kuchokera pa parishi ya Maula lati lili ndi chiyembekezo choti likwanitsa kufikira anthu ochuluka ndi ntchito zake za chifundo mu chaka chino cha 2024.
Wayankhula izi ndi wapampando wabungweli, mayi Artemisia Windo pambuyo pochita ntchito zachifundo kwa ma sisteri obindikira a Poor Clare ku Maula lero pa 09 March 2024.
Amayi Windo ati anachiwona chinthu chofunika kwambiri kuyamba utumiki wawo wogwira ntchito za chifundo mu chaka chino poyendera ma sisteriwa.
" Ife ngati Atumiki a Chifundo apa Maula tinachiona cha nzeru kuti 2024, utumiki wathu tiyambire kwa masisteri athu a kwa Poor Clare omwe timakhala nawo pompano. Amati 'Charity begins at home'," anatero Mayi Windo.
Bungwe la Atumiki Achifundo la pa parishi ya Maula lakhala likugwira ntchito za chifundo zosiyanasiyana monga kuyendera odwala m'zipatala, kuyendera ansembe komanso anthu achikulire.
Wolemba ndi Bro. Julius Collen Chalunda



Comments