Bungwe la Amayi aChikatolika kutsogolera chipembedzo m'chaka cha tsopano
- Edwin Sitima
- Jan 19
- 1 min read

Pamene chaka cha 2026 chayamba kumene, mabungwe komanso miphakati ya parishi ya Maula, yakangalika kupanga mapologalamu ofuna kuti atumikire ikafika nthawi yawo.
Nthawi ndi nthawi mabungwe komnaso miphakati imene ili pa parishiyi imatenga gawo pakutsogolera chipembedzo.
Limodzi mwa mabungwe omwe ayenditsa kale chipembedzo mchakachi ndi bungwe la amayi achiKatolika la CWA.
Loweruka pa 17 January 2026, amayiwa anakoza mu tchalitchi komanso kusamala malo ena.
Amayiwa sanalekere pomwepo ayi, tsiku la Mulungu anapereka mphatso za paguwa komaso kuwerenga mau.
Parishi ya Maula ndiyothokoza bungwe la amayi achiKatolikawa kamba kotsogolera chipembedzo.











Comments