AKHRISTU AKUMBUTSIDWA KUKHALA OKONDANA NDI ODZETSA MTENDERE MU NYENGO INO YA KHIRISMASI
- Edwin Sitima
- Dec 26, 2025
- 1 min read
Bambo mfumu a parishi ya Maula, bambo Francis Lekaleka, alimbikitsa akhristu pomwe akukondwelera nyengo ya Khirisimasi kukhala anthu okonda mtendere komaso chikondi ndi kuwala monga momwe Mulungu adachitira potumiza mwana wake Yesu Khristu.
Bambo Lekaleka ati anthu akuyenera kukondwelera ndi mtendere chifukwa kubadwa kwa ambuye Yesu kunabweretsa mtendere pakati pa anthu.

Iwo ati chikhiristu chimasowekera kukhala ndi mtendere komanso chikondi, kudzichepetsa monga momwe zidachitikira pa kubadwa kwa Yesu kudzera mwa Maria pamene malo anasowa.
"Tikuyenera kukhala anthu odzipereka panyengo ino yakubadwa kwa Yesu pomagawana zithu zomwe tili nazo, Yesu Khritsu anabwera kudzapatsa anthu mtendere pakati pa anthu a mitundu yonse ndiye zomwe tili nazo tikuyenera kudzipereka mwachikondi kwaonse," anatero bambo Lekaleka.
Bambo mfumuwa anapitiriza kunena kuti kubadwa kwa Yesu Khristu kudapereka mtendere ndi chimwemwe kwa abusa amene anali opanda kanthu komanso omwe amatengedwa ngati anthu osafunikira.
"Chimenechi chikupereka tathauzo lenileni lakubadwa Kwa Ambuye yesu. Anadzichepetsa polola kuti abusa aja akhale anthu wamba amene analibe kanthu koma analandira chimwemwe chimene Mulungu analonjeza kuti adzawachitira anthu ake. Mtendere ndi chikondi sizimawoneka pamene munthu uli wekha koma zimawoneka ndi anthu ena pomagawana zomwe tili nazo ndiye tikuyenera kulimbikitsa akhritsu kuti tikhale olumikizana ndi chimwemwe chenicheni mwa Khristu Yesu."
Ndipo mawu ake, wachiwiri wapampando wa parishiyi, Thomas Mbalule, ati
Khirismasi ndi tsiku lofunika kwambiri makamaka kwa ife akhristu.
Iwo anati: "Akhristu akuyenera kudziwa kuti ambuye Yesu atibadwira tonse komanso tikuyenera kudziwa tathauzo la mawu oti 'JOY' akutathauza kuti kutsogoza ambuye Yesu, tiyang'ane anthu ena komanso ifeyo patokha tikhale anthu odzetsa chimwemwe."















Comments