Ana 1 Miliyoni Kupemphera Kolona mu Dinale ya Maula
- Edwin Sitima
- Oct 7
- 1 min read
Ana a Tilitonse ochokera ku Maula Cathedral apemphera nawo Kolona wa Ana okwana 1 million ku Parish ya St. Dennis Ssebbugwawo - Chinsapo mu Arkidayosizi ya Lilongwe.
Chaka ndi chaka ana okwana 1Million pa dziko lonse la pansi amapephera kolona.
Kolona amapepheredwa pa 18 October koma chaka chino kolonayi wapepheredwa pa 7 October kamba koti ndi tsiku lomwe lidayamba kupempheredwa mchaka cha 2005 zomwe zikutanthauza kuti papita zaka 20 chiyambireni kupempheredwa.
Mwana wochokera ku Maula Cathedral, Thokozile Soko anawerenga ndi kutsogolera khumi lachiwiri.














Comments