Bungwe La Marriage Encounter Lalimbikitsa Ma Banja Atsopano Kulowa Bungweli
- Edwin Sitima
- 5 days ago
- 1 min read
Bungwe la mabanja la Marriage Encounter mu Arkidayosizi yaKatolika ya Lilongwe lalimbikitsa mabanja achinyamata kulowa bungweli ndi cholinga chofuna kuti adzilimbikitsika pa nkhani za banja ndi uzimu.
Banja la bambo ndi Mayi Kalulu omwe ndikhala pakati wa bungweli mu ma dayosizi a Lilongwe ndi Dedza, ndilo lapereka pempholi ku Maula Cathedral, pambuyo pamwambo wa nsembe ya Misa yopempherera mamembala ake omwe adatisiya.
"Tikupepha ma banja achinyamata omwe akwanitsa zaka zitatu ali m'banja kuti alowe bungweli, chifukwa timalimbikitsa chikondi pakati pa mamuna ndi mkazi, komaso mpingo," iwo anatero.

Mwazina, banjali lati pali masophenya ofuna kufikira madera ena omwe bungweli silokhazikika muchaka chikubwerachi.
"Ife abungwe la Marriage Encounter ndi khumbokhumbo lathu kuti tifikire ma parishi a ma boma ena monga ku Dowa, ku Nanthomba Parishi komanso ku Salima kumene Marriage Encounter silinakhazikike kwenikweni m'chigawo chino chapakati."
Bungwe la Marriage Encounter linayamba mu chaka cha 1985 kuno ku Malawi, ndipo limagwira ntchito zosiyanasiyana mu mpingo zomwe ndikuphatikizapo ntchito za chifundo.



Comments