CHAKA CHA EPIFANIA KU MAULA PARISHI
- Edwin Sitima
- Jan 5
- 1 min read
Bambo mfumu a parishi ya Maula, bambo Francis Lekaleka alimbikitsa ana a Tilitonse pa parishiyi kukhala okonda kupemphera komanso ophathana ndi mulungu nthawi zonse
Bambo Lekaleka alankhula izi Lamulungu pa mwambo wa nsembe ya Ukalistiya ya Epifaniya pa parishiyi.

Bambo Lekaleka kuwerenga uthenga wabwino
Apa Iwo ati Epifaniya ya chaka chino ithandizire kusintha miyoyo ya anawa pomweso pano alowa chaka chatsopano.
Bambo Lekaleka akumbutsaso makolo kuti alimbikitse anawa kukonda moyo wopemphera ndi cholinga chofuna kuwathandizira kuyenda m'moyo wa chikhristu nthawi zonse ndi kutenga chitsanzo chabwino cha Maria ndi Yosefe cholimbikitsa anawa kuti adziphathana ndi Yesu Khristu nthawi zonse.

Mwazina, Iwo ati akulingalira zokonza njira zoti anawa adzitenga nawo gawo m'zochitika zosiyanasiyana monga kupembedza ambuye Yesu okhala mu Ukalistiya komanso kutsogolera mapemphero a Kolona.
Liwu lakuti Epifaniya limachokera ku Chigiriki ndipo limatanthauza kuti kuonekera kwa Mulungu pakati pa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
Nyengoyi imakumbukiranso kubwera kwa anzeru aku m'mawa amene amatchedwanso Akatswiri a Nyenyezi aku Mmawa (The Magi).



















Comments