La Mulungu La Chifundo cha Mulungu ku Maula Cathedral
- Communications
- Apr 12
- 1 min read
Bungwe la Chifundo cha Mulungu pa parishi ya Maula lachita nawo chaka cha la Mulungu la Chifundo cha Mulungu lero pa 12 April 2026.
Mwambo wa nsembe ya chakachi unatsogoleredwa ndi bambo Peter Makina.
Mu ulariki wawo, bambo Makina anapempha akhristu kukhala okonda kuthandizana nthawi zonse kuphatikizapo pa mavuto osiyanasiyana ndipo kuti adzichita izi ndi chikhulupiliro.

"Tiyeni akhristu tithandiza anzathu. Kodi Ife timachita zotani? Kodi ine ndimamvera chifundo anzanga? Tiyeni tichitire chifundo azathu kuti nawonso akachitire chifundo ena" anatero bambo Makina.
Iwo apemphanso akhristuwa kuleka kukhala okaika ndikukhala anthu okhupilira nthawi zonse. Bambo Makina ati akhristu "tikamalandira Ukaristia tidziti 'ndikukhulupiliradi ambuye Yesu okhala mu Ukaristia.'
Ndipo pomaliza, iwo apempha akhristu kuthandiza anthu omwe ndi osowa kuphatikizapo omwe amapempha minsewu posatengera mphulupulu zawo,
"Amene akuvutika aja tiwathandize posatengera zochita zawo, monga ana a m'misewu tisatengere kuti amaba koma tiwathandize ndipo tisatope kuchita zabwino," anamaliza motero bambo Makina

























Comments