Maula Parishi Yalandira Bambo Mfumu Atsopano
- Edwin Sitima
- Dec 15, 2025
- 1 min read
Akhristu ku Parishi ya Maula lero pa 15 December 2025 alandira abambo mfumu awo atsopano, bambo Francis Lekaleka, pa mwambo wa nsembe ya ukalistiya ya m'mawa.
Mwambowu omwe umachitikira ku parishiyi, umatsogoleredwa ndi bambo Louis Chikanya omwe akuchoka pa parishipa ngati bambo mfumu kupita kukatumikira kunja kwa dziko lino, mothandizana ndi bambo Geofrey Chikapa omwe amatumikira ngati bambo mthandizi wa parishi pomwenso akukatumikira ku parishi ya St. Anthony of Padua ku Area 25.
Bambo Chikanya afunira mafuno abwino bambo Lekaleka pomwe akhale akuyamba ntchito yawo ngati bambo mfumu watsopano.
Mmawu awo, amayi Dorica Chirwa omwe ndi wapampando wa parishiyi, ndipo amayakhula malo mwa akhristu onse, ati bambo Lekaleka alandilidwa ndipo agwira anawo ntchito bwino.
"Malo mwa akhrsitu onse, komanso parish council yonse, bambo ndikufuna kukulandirani ndi manja awiri, komanso kukumasulani kuno Ku Maula Parish."

Ndipo pamapeto, amayi Chirwa anafunira ulendo wa bwino bambo Chikanya komanso bambo Chikapa pomwe akupita kukatumikira madera ena.









Comments