"Ukaristiya Thupi ndi Magazi a Ambuye yesu"
- Communications
- Jun 8
- 1 min read
Akhristu kuchokera pa parishi ya Maula alangizidwa kukhala anthu okonda kulandira Ukaristia nthawi zonse.
Bambo Peter Makina ndi omwe alankhula izi kudzera mu ulaliki wawo pa mwambo wa nsembe ya Misa ya Chaka Cha Ukaristia.
Bambo Makina anati akhristu akalandira thupi la Ambuye Yesu moyo wawo udzisinthika popeza "Ukaristia azifanafana ndi Yesu mwini popeza munthu aliyense amakhala chomwe amadya."
Ndipo iwo anaonjezera kuti akhristu asanalandire ukaristia, akuyenera kuyamba kukonza mu mtima mwawo polandira sakamenti la kulapa, kuti ambuye apeze mtima muli bwino.
Bambo Makina anapitilira kupempha akhristu kuti adzipita nthawi yabwino ku mwambo wa nsembe ya Ukaristiya chifukwa anthu ena amapita mwachangu ku misokhano ya ndale angakhalenso ku mpira, pomwe ku tchalitchi timachedwa.
Pomaliza, iwo anatsindika kuti Ukaristia umalimbikitsa moyo wa chikhristu chifukwa ndi chakudya cha uzimu.



Comments