top of page
Search

ULARIKI WA PA 05 APRIL 2026, LAMULUNGU LA CHAKA CHA PASAKA

Updated: Apr 7


Abale ndi alongo okondedwa, Lero tikuyima pano ndi uthenga umodzi wokha, koma waukulu kuposa zonse: Khristu wauka! Inde, wauka ndithu! Aleluya!


Mu Uthenga Wabwino wa lero, Yohane akufotokoza za Mariya wa Magadala amene anapita ku manda m'mawa kwambiri. Atafika, anaona mwala wachotsedwa. Ndipo anathamanga kukamuuza Simon Petro NDI wophunzira uja amene Yesu ankankonda kwambiri. Ndipo ones awiri anathamanga, koma wophunzira wina uja anathamanga kuposa Petro. Atafika kumanda Anaona manda analibe kanthu, nsalu zomwe anamukutira nazo Yesu zinali pamenepo, ndipo nsalu yomwe anamukulungira kumutu, kanali pakokha kopindapinda. Onse anali ozizwa.


Ndi Chifukwa chiyani nsalu yakumutu ija inali yopindidwa bwino? Mu Uthenga Wabwino, Yohane akufotokoza mwatsatanetsatane kuti:

nsalu zina zinali pansi, koma nsalu ya kumutu inali payokha, yopindapinda Izi sizinalembedwe mwangozi. Zili ndi tanthauzo lalikulu.


1. Poyamba zikusonyeza kuti Ambuye Yesu sanachite kubedwa.

Ngati munthu akanaba thupi la Yesu: sakanakhala ndi nthawi yopinda nsalu bwino,

akanangotenga thupi mwachangu ndi kuthawa. Koma pano tikuwona dongosolo osati chisokonezo. Izi zikusonyeza kuti zimene zinachitika si ntchito ya anthu, koma ntchito ya Mulungu.


2. Kachiwiri Chizindikiro cha kuuka, osati kubwerera ku moyo wakale

Pamene Yesu anaukitsa Lazaro, Lazaro anatuluka ali womangiridwabe ndi nsalu—amafunika anthu kuti amumasule. Koma Yesu: sanatuluke ngati munthu wobwerera ku moyo wakale, koma anauka ndi moyo watsopano, waulemerero. Choncho nsalu zotsalira zikuwonetsa kuti: Yesu wasiya imfa kwathunthu. Komanso ndiye kuti iye ndiye kuuka komanso oukitsa anthu KWA akufa nchifukwa chake sanasowekere anthu ena kuti amasule nsalu zomwe anamukulungira.


3. kachitatu Chizindikiro cha mtendere ndi ulamuliro

Nsalu ya pamutu itakulungidwa bwino ikusonyeza kuti: panalibe mantha, panalibe kuthawa, Yesu anachita zonse mwamtendere ndi ulamuliro.


4. kachinayi Tanthauzo la chikhulupiriro kwa ife

Ichi ndichifukwa chake Yohane ataona izi, anakhulupirira. Sanangoona manda opanda kanthu, koma anaona zizindikiro za ntchito ya Mulungu. Anaona nsalu yopindapinda.

Kodi izi Kutanthauzanji kwa ife lero?


Abale ndi alongo, Nthawi zina Mulungu samalankhula ndi ife kudzera mu zozizwitsa zazikulu, koma kudzera mu zizindikiro zing’onozing’ono koma zomveka bwino. Nsalu inapindidwa bwino ija ikutiuza kuti: Mulungu ali ndi dongosolo pa moyo wathu,

ngakhale pamene zinthu zikuwoneka ngati zasokonekera. Choncho Pasaka ikutiuza kuti: Imfa sinapambane. Yesu ali moyo—ndipo zonse zili m'manja mwake.

Abale NDI alongo tamva kuti Mariya wakunmagadala ataona zidabwitsa ku Manda a Yesu anathamanga kukauza Petro ndi Yohane (ophunzira amene Yesu ankankonda kwambiri. Iwo nawonso akuthamangira ku manda. Yohane akuti: “Anaona, ndipo anakhulupirira.”


Abale ndi alongo, abale athuwa Anaona manda opanda kanthu… koma anakhulupirira chifukwa cha zomwe anaona. Palibe Yesu amene anaoneka pamenepo. Palibe mawu amene anamveka. Koma kuchokera pa zimene anaona—manda opanda kanthu, nsalu—mtima wawo unayamba kulimba mu chikhulupiriro.


Zimenezi zikutiphunzitsa kuti:

Mulungu amagwira ntchito ngakhale pamene ife tikuona kuti palibe chilichonse.


Nafe m'moyo wathu tili ndi “manda” osiyanasiyana:

pamene ndalama sizikukwanira pa banja,

pamene m’banja muli mikangano,

pamene achinyamata akusowa ntchito,

pamene munthu ali ndi matenda kapena akusowa chiyembekezo.

Nthawi zambiri timangoganiza kuti zinthu zasokonezeka, kapena kuti zatha. Koma uthenga wa Pasaka ukuti: pamene ife tikuona mathero kapena chisokonezo, Mulungu amaona chiyambi chatsopano.


Abale ndi alongo, Petro anaona—ndipo anadabwa. Yohane anaona—ndipo anakhulupirira. Kusiyana kuli pa mmene mtima umafotokozera zomwe taona. Nafe tikhoza kuyang’ana mavuto okha, kapena kuwona kuti Mulungu akugwirabe ntchito ngakhale pakati pa mavuto athu.


Ndipo ngati Khristu wauka, izi ziyenera kuwonekera m'moyo wathu wa tsiku ndi tsiku;

M’banja, ngati panali kusamvana, tiyeni tipite patsogolo ndi kulankhulana komanso kukhululukirana.


Kwa amene akuvutika ndi ndalama, tisataye mtima, koma tipitirize kugwira ntchito molimbika ndi kudalira Mulungu.


Kwa achinyamata omwe akusowa ntchito, tiyeni tipitirize ndi chiyembekezo osaleka kulimbikira.


Kwa odwala ndi omwe akuwasamalira, tidziwe kuti Mulungu ali pafupi ndipo sakusiya anthu ake.


Abale ndi alongo, lero sitikukondwerera manda opanda kanthu okha. Tikukondwerera kuti moyo wapambana imfa, chiyembekezo chapambana mantha, chikondi chapambana tchimo.


Choncho tiyeni lero: tisakhale anthu a manda, koma tikhale anthu a kuuka.

Tiyeni tichoke pano:

ndi mtima wokhululuka,

ndi chiyembekezo chatsopano,

ndi chikhulupiriro cholimba,

Ndipo pamene tikukhala motero, dziko lidzaona kuti Khristu ali moyo—ndipo izi zidzakhudza banja lathu, abale athu, komanso dera lathu lonse.


Khristu wauka! Inde, wauka ndithu!

Aleluya!


Ulariki wa abambo Peter Makina

 
 
 

Comments


ABOUT US

We are simply known as a Cathedral of Lilongwe, which is the Capital City of Malawi. We belong to the metropolitan Archdiocese of Lilongwe whose safragan dioceses are Dedza, Mzuzu and Karonga. We follow the Roman or Latin rite.

ADDRESS

+265 (0) 1 755 846

+265 (0) 998 73 35 93

P.O Box 1524, Lilongwe.

parishpriest@maulaparish.org

administration@maulaparish.org

SUBSCRIBE FOR EMAILS

Thanks for submitting!

  • Facebook
  • Instagram
  • Twitter

© 2025 by Team iWork. Proudly created with Wix.com

bottom of page