top of page
Search

Abambo a Bungwe la CMA Alimbikitsidwa Kuiika Chikhulupiriro Patsogolo M'malo mwa "Nthawi Zotanganidwa"


Bungwe la abambo la CMA la pa parishi ya Maula lapemphedwa kukhala lochilimika potumikira Mulungu komanso kupezeka kwa ma membala ake pa mikumano yomwe limakhala nayo.


Pempholi laperekedwa ndi wapampando wa bungweli, a Steve Chipala pambuyo pa mwambo wa nsembe ya Misa yotolera limodzi limodzi womwe unachititsidwa ndi bungwe la abambo, mu Arkidayosizi ya Lilongwe ku parishi ya St. Kizito, Chigoneka.


Mwambo wansembe ya Misayi unatsogoleredwa ndi Episkopi mthandizi wa Arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Vincent Mwakhwawa omwe analimbikitsa abambowa kumakhala patsogolo ndikuganizirapo za udindo wawo potukula mpingo pomwenso dziko lino likhale likukondwelera zaka 125 zakupezeka kwa mpingo wachiKatolika kuno ku Malawi chaka chino.

Chipala, wapampando wa bungwe la abambo la CMA pa Parishi ya Maula
Chipala, wapampando wa bungwe la abambo la CMA pa Parishi ya Maula

A Chipala ati uthenga wa ambuye Mwakhwawa wa lero uthandizire kusintha abambo ambiri kuti asunthire chifupi ndi Mulungu pofuna kumanga mpingo wamphamvu.


Iwo ati zimakhala zokhumudwitsa nthawi zambiri kuona abambo ambiri asakutenga nawo mbali muzochitika za mu mpingo ponena kuti amakhala otanganidwa.


"Tiyeni a zibambo anzanga tichilimike potenga nawo gawo mu zochitika za mu mpingo pofuna kumanga mpingo wa mtsogolo," anatero a Chipala.


Bungwe la abamboli lachita mwambowu ndicholinga chofuna kupeza ndalama za msonkhano wa bungweli mdziko muno wapachaka womwe udzachitikire mu Arkidzayosiziyi mwezi wa March.


Wolemba ndi Peter Dumayo

 
 
 

Comments


ABOUT US

We are simply known as a Cathedral of Lilongwe, which is the Capital City of Malawi. We belong to the metropolitan Archdiocese of Lilongwe whose safragan dioceses are Dedza, Mzuzu and Karonga. We follow the Roman or Latin rite.

ADDRESS

+265 (0) 1 755 846

+265 (0) 998 73 35 93

P.O Box 1524, Lilongwe.

parishpriest@maulaparish.org

administration@maulaparish.org

SUBSCRIBE FOR EMAILS

Thanks for submitting!

  • Facebook
  • Instagram
  • Twitter

© 2025 by Team iWork. Proudly created with Wix.com

bottom of page