Sukulu ya Mlale Minor Seminale iyendera Parish ya Maula
- Edwin Sitima
- Jun 14
- 1 min read
Ophunzira ochokera ku sukulu ya St. Paul Minor Seminary - Mlale mu Arkidayosozi ino ya Lilongwe alimbikitsidwa kukhala okonda maphunziro awo.
Izi zayankhulidwa ndi a Chapola, omwe ndi wapampando wa akhristu omwe amapephera Misa ya Latin ku Maula Cathedral.
A Chapola ati ali ndi chiyembekezo kut ena mwa anyamatawa adzakhala ansembe, poti munda wakula achepa ndi ntchito.
"Inu achinyamata limbikirani maphunziro anu kut ena mwa inu mudzatumikire Mulungu.
Ndipo bambo Peter Makina anathokoza ophunzirawa chifukwa chodzapemphera nawo ku Maula Cathedral.
Ophunzirawa anapemphera ndi kuyimbira pa mwambo wa nsembe ya Misa ya Latin ku Maula, ndipopamapeto pa nzonse iwo anacheza ndikudyera pamodzi ndi akhristu ngati banja limodzi.
Misa ya Latin ku Maula Cathedral imakhalapo kamodzi Lamulungu loyamba la mwezi uli onse.





















Comments