top of page
Search

ANA A TILITONSE OCHOKERA KU MAULA PARISH ACHITA NTCHITO ZA CHIFUNDO PA NDENDE YA MAULA (LILONGWE)

Loweruka pa 28 March 2026, ana a Tilitonse ochokera pa parishi ya Maula apereka thandizo la zinthu zosiyanasiyana pa ndende ya Maula mu mzinda wa Lilongwe.


Anawa akwanitsa kuYendera ana anzawo omwe ali mndende ngati njira imodzi yochita za chifundo mu nyengo ino ya lenti.



M’mawu awo, ena mwa ana a Tilitonse ochokera pa parishiyI, Stephano Mavuto komanso Giniya  Sibino ati kupita ku ndende ya Maula kwakhala kowathandiza kugawana ndi anzawo za maphunziro omwe amaphunzira ku tchalitchi maka pochitira chifundo anthu ena.


Stephano Mavuto ndi Giniya  Sibino kuyankhulapo pa momwe ayendera ku ndende ya Maula
Stephano Mavuto ndi Giniya  Sibino kuyankhulapo pa momwe ayendera ku ndende ya Maula

Mmawu awo, a Steve Chipala omwe ndi mmodzi mwa aphunzitsi a ana a Tilitonse pa Parishi ya Maula, ati anaona kuti kunali koyenera kutenga ana a Tilitonse kuti akaone ana anzawo omwe ali pa ndende ya Maula popeza kuti anthu osiyanasiyana amapita kukaona magulu anzawo popereka chitsanzo cha amayi kuti amapita kukaona amayi anzawo.


A Chipala kufotokonzera za ubwino oyendera a ndende posasankha zaka kapena gulu la anthu
A Chipala kufotokonzera za ubwino oyendera a ndende posasankha zaka kapena gulu la anthu

A Chipala ati kupita kwa ana a Tilitonse ku ndendeyi kuwathandiza kukhala ozindikira kuti aliyense olakwa amamangidwa posatengera zaka zake ndipo ati izi ziwathandiza anawa kukhala ochita zinthu zoyenera nthawi zonse.


Pamwambo opereka zinthuzi, ana a Tilitonse anasangalatsanso apandendewa ndi kuchita sewero komanso kuimba zomwe malingana ndi a Chipala, zithandizira apandendewa kukhala ndi chikhulupiliro ngati chinali chotayika komanso kuwachotsera nkhawa.


"Lekani ana abwere"

Ndipo a pandendewa ati ali ndi chisangalalo pomwe alendo omwe anali nawo lero awasangalatsa ndipo ati akhala osinthika popeza nawo ndi a chichepere.


"Ana atumiki"

Andendewa apempha ana anzawo omwe ali kunja kwa ndende kukhala osamalitsa pakachitidwe ka zinthu maka kuonetsetsa kuti sakuchita zosemphana ndi malamulo a Mulungu.


Ana a Tilitonse ochokera pa parishi ya Maula apereka thandizo la sopo, mafuta ndi zina.

 
 
 

Comments


ABOUT US

We are simply known as a Cathedral of Lilongwe, which is the Capital City of Malawi. We belong to the metropolitan Archdiocese of Lilongwe whose safragan dioceses are Dedza, Mzuzu and Karonga. We follow the Roman or Latin rite.

ADDRESS

+265 (0) 1 755 846

+265 (0) 998 73 35 93

P.O Box 1524, Lilongwe.

parishpriest@maulaparish.org

administration@maulaparish.org

SUBSCRIBE FOR EMAILS

Thanks for submitting!

  • Facebook
  • Instagram
  • Twitter

© 2025 by Team iWork. Proudly created with Wix.com

bottom of page