Chaka chokondwera nkhonswe ya dinale ya Maula mu Arkidayosizi ya Lilongwe mchaka cha 2026
- Edwin Sitima
- May 3
- 1 min read
Loweruka pa 2 May 2026, akhristu ochokera m'ma parishi omwe ali pansi pa dinale ya Maula, mu Arkidayosizi ya Lilongwe anasonkhana ku parishi ya St. Denis Ssebuggwawo (Chinsapo) komwe kunachita chaka chokondwerero nkhoswe ya dinale yawo "Amai Maria, Amayi a ku Africa (Our Lady of Africa)."

Dinale ya Maula ili ndi ma Parish asanu ndi awiri omwe ndi kuphatikizapo Maula Cathedral, St. Denis Ssebuggwawo (Chinsapo), St. Kizito (Chigoneka), St. Padre Pio (New Gulliver), Maria Mthandizi wa Akhristu (Mtandire), St. Patrick's ( Area 18) komanso St. Ignatius (Area 30).
Ambuye mthandizi a Arkidayosiziyi, ambuye Vincent Mwakhwawa ndi omwe anatsogolera mwambo wa nsembe ya Ukaristia yokondwelera nkhoswe ya dinaleyi.

Ambuye Mwakhwawa anapempha akhristu mu dinaleyi kuti akhale anthu okonda Kupemphera mapemphero a Kolona komanso kukhala okonda kupembedza Yesu okhala mu ukaristiya.

Pomwe dinale ya Maula ili imodzi mwa ma dinale omwe akupezeka mkwatikati mwa mzinda wa Lilongwe, ambuyewa anapempha dinaleyi kukhala yachitsanzo kwa akhristu ena komanso ma dinale ena.
Pambuyo pa mwambo wa nsembe ya Misa Kunali zochitika za msangulutso zosiyanasiyana monga magule amakolo, ndakatulo komanso masewero a mpira.























Comments