top of page
Search

Lamulungu La Mayitanidwe ku Parishi ya Maula m'chaka cha 2026

Achinyamata awapempha kumvetsera ndi kuyankha mayitanidwe awo moyenera omwe Mulungu akuwayitanira.


Bambo Peter Makina ndi omwe ayankhula izi pa mwambo wa nsembe ya Ukaristiya ya chaka cha mayitanidwe, ku Maula Cathedral mu Arkidayosizi ya Lilongwe.


Bambo Makina
Bambo Makina

Bambo Makina anati makolo ali ndi ntchito yambiri yothandiza ndi kulimbikitsa achinyamata kut ayankhe mayitanidwe oyenera, monga moyo wa unsembe, ubulazala, uSisteri komaso moyo wa m'banja, komaso moyo okhala pa yekha.


"Makolo tiyeni tikhale abusa abwino, polimbikitsa ana kutumikira Mulungu mwa njira yosiyanasiyana, m'busa wabwino amamva fungo la nkhosa zake."


Mpingo waKatolika pa dziko lonse lamulungu lachinayi mu nyengo ya Pasaka umakumbutsa achinyamata kuti amve mayitanidwe otumikira Mulungu potsatira mapazi a yesu Khristu yemwe ndi m'busa wabwino.



Pa Mwambo wa nsembe ya Ukaristiya, kwaya ya Bunda Catholic Alumni, ndiyomwe inatsogolera maimbidwe ndipo wapampando wa chipembezo pa parish ya Maula anathokoza kwayayi kamba ka utumiki wake.




 
 
 

Comments


ABOUT US

We are simply known as a Cathedral of Lilongwe, which is the Capital City of Malawi. We belong to the metropolitan Archdiocese of Lilongwe whose safragan dioceses are Dedza, Mzuzu and Karonga. We follow the Roman or Latin rite.

ADDRESS

+265 (0) 1 755 846

+265 (0) 998 73 35 93

P.O Box 1524, Lilongwe.

parishpriest@maulaparish.org

administration@maulaparish.org

SUBSCRIBE FOR EMAILS

Thanks for submitting!

  • Facebook
  • Instagram
  • Twitter

© 2025 by Team iWork. Proudly created with Wix.com

bottom of page