top of page
Search

ATSOGOLERI A BUNGWE LA CWA AKUMANA NDI BAMBO MFUMU


Atsogoleri a bungwe la amayi a chiKatolika la CWA, pa parishi ya Maula anakumana ndi bambo mfumu a parishiyi, Bambo Francis Lekalek, lamulungu pa 22 February 2026 ndi cholinga chofuna kuwadziwitsa za atsogoleriwa komanso kudziwa ntchito zimene bungweli limagwira, zovuta zimene bungweli limakumana nazo komanso mmene bungweli limagwira ntchito ndi ma bungwe ena.


Adindowa anafotokozerapo zambiri za bungweli monga kusonkha ndalama zofunika kuyendetsa bungweli, kuyendetsa chipembedzo, kutumikira ntchito za chifundo komanso kulumikizana bwino ndi dinale ya Maula.


Amayiwa anafotokonzeraponso za kuchepa kwa a mayi omwe amabwera ku misonkhano ya pa mwezi komanso kukakhala zochitika za parishi.


M'mawu awo, bambo Lekaleka anati mikumano ya amayi ndi yofunika kwambiri kuti bungweli lidziyenda bwino.


Iwo analangizanso amaiwa kuti achilimike pa njira za uzimu wao maka popanga mibindikiro ndikuwalangiza kuti apange mwachangu mlozo wa chaka chino cha 2026 kuti zonse ziziyenda mu ndondomeko yake.

 
 
 

Comments


ABOUT US

We are simply known as a Cathedral of Lilongwe, which is the Capital City of Malawi. We belong to the metropolitan Archdiocese of Lilongwe whose safragan dioceses are Dedza, Mzuzu and Karonga. We follow the Roman or Latin rite.

ADDRESS

+265 (0) 1 755 846

+265 (0) 998 73 35 93

P.O Box 1524, Lilongwe.

parishpriest@maulaparish.org

administration@maulaparish.org

SUBSCRIBE FOR EMAILS

Thanks for submitting!

  • Facebook
  • Instagram
  • Twitter

© 2025 by Team iWork. Proudly created with Wix.com

bottom of page