ZOCHITIKA PA LOWERUKA LOYERA KU MAULA PARISHI MCHAKA CHA 2026
- Edwin Sitima
- Apr 4
- 1 min read
Updated: Apr 5
Tsiku la loweruka loyera ndi tsiku lomwe akhristu a mpingo waKatolika amakumbukira kuuka Kwa ambuye Yesu pa dziko lonse lapansi.
Parishi ya Amai a ku Afrika - Maula mu Arkidayosizi ya Lilongwe, inachitanso chimodzimodzi motsogozedwa ndi abambo Peter Makina, mwambo omwe unayamba ndi kuyatsa komanso kudalitsa moto, ndipo unakapitira mu tchalitchi cha Maula ndi kuyatsa makandulo.
Mu ulaliki wawo, bambo Makina anatsindika kuti monga khristu wauka wakufa, ifenso omutsata tikuyenera kusintha makhalidwe athu akale pakuti iye amene anaikidwa m'manda wauka kwa akufa ndipo kuti ifa yagonjetsedwa.
"Tiyeni nthawi zonse tipewe makhalidwe oipa omwe amatiyika mu mdima ngati machimo," anatero bambo Makina.
Mwambo wa Loweruka Loyera umagawidwa zigawo zinayi; Chigawo choyamba ndichodalitsa moto, chachiwiri ndi chowerenga mau, chachitatu ndi chigawo chobwereza malumbilo a ubatizo komanso chigawo chachinayi chomwe ndi chigawo cha nsembe ya Misa.
Mu chigawo chakuwerenga mawu oyera, mau oyerawa anachokera ma buku awa: Genesisi 1:1-22, Mau achiwiri Eksodo 14:15-15:1, achitatu anachokera buku la mneneri Yesaya 54:5-14, mneneri Baruki 5:9-15,34:4, Ezekiel 36:16-17a,18-28, kalata ya Paulo Kwa Aroma 6:3-11ndipo uthenga wabwino unachokera m'buku la Luka 24:1-12.
Mwambowu umachitika chigawo chakumadzulo panthawi yomwenso ku makhala m'bindikiro wakuukanso kwa Yesu Khristu. Ndipo mmawa wa lowerukali pa 04 April 2026, bungwe la achinyamata pa parishiyi linali kalikiliki okonzekera za mwambowu maka pogwira ntchito limodzi powaza nkhuni.
Wolemba ndi Edwin Sitima

























Comments